Pinned Tweet
Follow the Channel Africa Chinyanja channel on WhatsApp: whatsapp.com/channel/0029Vb8…
Yemwe anatsogolera chipani cha National Reconciliation Party for Unity and Prosperity -NRPUP pa masankho omwe anachitika ku Zambia mu mwezi wa August chaka chino, Brian Mundubile ndi yemwe anaima ngati wachiwiri wake Makebi Zulu, pamodzi ndi ena khumi ndi awiri,
2
32
Atsogoleri a maiko a Kenya ndi Democratic Republic of Congo, William Ruto ndi Felix Tshisekedi motsogozana, agwirizana za kufunika kugwira ntchito limodzi molemekezana pa kufuna kulimbikitsa ubale m'magawo osiyana siyana.
2
17
Adindo pa nkhani za ngozi zogwa mwa dzidzidzi ku Nigeria ati tsapano apeza matupi a anthu okwana 29 omwe amwalira pa ngozi ya kumira kwa bwato.
Izi ndi malingana ndi bungwe la National Emergency Management Agency lomwe lati anthuwa anali Pa ulendo opita ku maliro.
1
8
Nduna ya zachuma mdziko la Malawi a Joseph Mwanamvekha ati thumba la ndalama lomwe boma lasayinira ndi mayiko komanso nthambi zomwe zimathandizira dzikolo lithandizira kuti boma lichepetse mavuto akusowa kwa mafuta a galimoto.
3
27
Patadutsa miyezi yoposa isanu ndi umodzi chiyambireni pa nthawi yomwe matenda a Ebola anayamba kufalikira mdziko la DRC, akatswiri pa nkhani za sayansi akupitilira kuchita kafukufuku pa kufuna kumvetsetsa chomwe chikupangitsa kupitilira kofalikira kwa matendawa.
1
23
Dziko la Malawi, lasaina mgwirizano ndi dziko la Tanzania pa nkhani yotumiza odwala kukalandira thandizo kudzikolo. Maiko awiriwa asaina mgwirizanowu pa mwambo wapadera mu mzinda wa Dar es Salaam pomwe nduna za umoyo zati izi zithandiza a Malawi omwe akufunika thandizo lapadera.
1
38
Bungwe loona zipata mdziko la South Africa la Border Management Authority, lati nthambi pansi pa bungweli lotchedwa BMA Integrity Unit, lamanga anthu asanu omwe akuganiziridwa kuti akudzidwa pa mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu pa chipata cha Van Rooyens Gate.
1
33
Lipoti latsopano lomwe latulutsidwa ndi bungwe lodziimilira palokha lotchedwa Swiss Aid, lapeza kuti boma la dziko la United Arab Emirates ndi lomwe linatsogola pa nkhani ya mwala wa mtengo wapatali wa golide kufika mdzikolo kuchokera ku Africa mu njira zosabvomelezeka. Izi,
1
31
Bungwe loona zipata mdziko la South Africa la Border Management Authority, lati likulimbikira pa zintchito zofuna kuthana ndi mchitidwe wa kuzembetsedwa kwa katundu monga magalimoto kulowa mmaiko oyandikana ndi dzikoli mosabvolezeka. Bungweli, lati zipata za dzikoli,
2
40
Pali chiyembekezo kuti zipani zomwe zinatenga nawo gawo pa masankho a maboma aang'ono ang'ono mdziko la South Africa, akhazikitsa maboma a migwirizano kumapeto kwa sabata lino. Izi, ndi malinga ndi mlembi wamkulu wa chipani cha EFF Marshal Dlamini,
1
17
Boma la dziko la South Africa, laperaka chenjezo kwa kazembe watsopano wa dziko la Nigeria, Femi Fani- Kayode. Chenjezoli, lomwe limatchedwa demarche, ndi chidzudzulo chomwe chimaperekedwa ndi maboma kwa a kazembe kapena nthumwi za maiko ena pakakhala kusamvana.
1
42
Wamkulu wa zintchito za asilikali mdziko la Uganda, General Muhoozi Kaneirugaba, waopseza atolankhani kuti atha kumaphika ndende akapezeka olakwa pa kufalitsa nkhani zonyoza prezidenti Yoweri Museveni ndi banja lake. Gen Kaneirugaba, yemwe ndi mwana wa prezidenti Museveni,
1
575
Prezidenti wa dziko la USA Donald Trump, wafika mdziko la Phillipines komwe ali pa ulendo wa ku maiko a ku Asia. Trump, akuyembekezeka kukafikanso ku dziko la China pa ulendowu omwe ndi wa masiku angapo. Iye, watenganso nawo gawo pa tsiku lomaliza la msonkhano wa atsogoleri a
1
32
Kampani ya zintchito za mafuta ya mdziko la Nigeria ya Dangote Refinery, yati ili ndi cholinga chogulitsa gawo la kampaniyi kwa anthu wamba lokwera ndi 30 percenti pa kufuna kupeza ndalama zokwana $2.1 biullion. Kampaniyi, yati ndalamayi ithandizira pa kufuna kukweza ndi
1
17
Bwalo la milandu mdziko la Guinea, lapereka chilango kwa anthu oposa 200 omwe apezeka olakwa pa milandu yogwira zintchito pa migodi ya miyala ya golide mosabvomelezeka. Poperka chigamulochi, bwaloli lati mchitidwe wa anthuwa unapangitsa kuti za chilengedwe zionongeke.
1
13
Bwalo lalikulu la milandu mu mzinda wa Johannesburg mdziko la South Africa, lati lipereka chigamulo posachedwa pa nkhani yokhudza anthu othawa kwawo omwe ali mdzikoli omwe pakadali pano ali m'manja mwa adindo. Bwaloli, lakhala likumva nkhaniyi kwa masiku awiri potsatira bwalo la
2
37
Anthu okhala mu dera la Protea Glen mtauni ya Soweto kummwera kwa mzinda wa Johannesburg mdziko la South Africa, usiku wapitawu anachita zionetsero zofuna kuonetsa kusasangalatsidwa ndi kusowekera kwa madzi. Anthuwa, anaotcha matayala, ndipo anatseka misewu yolowera mu tauniyi.
Zionetsero zomwe bungwe la HRDC linakonza kuti zichitike lero mdziko la Malawi , zalephereka.
Wapampando wa bungweli, Michael Kaiyatsa, wati bungweli layimitsa zionetserozi pambuyo poyankhulana ndi Polisi pomwe apolisiwa anena kuti saakwanitsa kupereka chitetezo chawo.
2
32
Bungwe loona za masankho mdziko la Gambia, la Independent Electoral Commission, laloleza prezidenti wa dzikolo Adama Barrow kudzaima nawonso pa masankho osankha mtsogoleri pamodzi ndi ena asanu ndi atatu. Aka, kakhala kachitatu Barrow kuima nawo pa masankho, ndipo masankhowa
2
26



